Title: Mundubile na Makebi
(Chorus)
Mundubile na Makebi, tiyomboleni ku mdima,
Banatipeleka mu usiku, tating'amba kulirira.
Mundubile na Makebi, tiyatsileni nyale,
Tione poponda bwino, chitukuko chifike kale.
Ku Mongu, ku Solwezi,
Ku Livingstone na Kaputa,
Tiyatsileni nyale, chitukuko chilowe m'zipata.
(Verse 1)
Banatilonjeza mbandakucha, dzuwa lidzawala,
Koma kholoko yaima pa zero, nthawi siyiyenda.
Anati zinthu zisintha, moyo uzakhala bwino,
Koma lero tikufunsa, kodi lonjezolo lili kuti?
(Chorus)
Mundubile na Makebi, tiyatsileni nyale,
Tione poponda bwino, chitukuko chifike kale.
Ku Mongu, ku Solwezi,
Ku Livingstone na Kaputa,
Tiyatsileni nyale, chitukuko chilowe m'zipata.
(Verse 2)
Banati nkhuku tizadya, unga ukhale wotsika,
Fuel na dollar zibwerera, moyo ukhale wosavuta.
Koma lero mdima wokha, malonjezo anangotha,
Tatsala ndi mafunso ambiri, mayankho palibe.
(Verse 3)
Beve kwao chabe ophunzira, m'ma province onse,
Police commissioners ambiri, ochokera mbali imodzi.
Data base recruitment inayima, achinyamata akuyembekezabe,
Asiliza sukulu kalekale, ntchito azilowa liti?
(Chorus)
Mundubile na Makebi, tiyatsileni nyale,
Tione poponda bwino, chitukuko chifike kale.
Ku Mongu, ku Solwezi,
Ku Livingstone na Kaputa,
Tiyatsileni nyale, chitukuko chilowe m'zipata.
(Verse 4)
Migodi inagulitsa, anthu akufunsa chifukwa,
Ndalama zikupita kuti? ndani akupindulapo?
Lero m'misasa ya campaign, mawu akuchuluka,
Koma anthu aku Magoye akufunsa, "Tawama pati?"
(Final Chorus)
Mundubile na Makebi, tiyomboleni ku mdima,
Tiyatsileni nyale lero, tione njira ya mawa.
Ku Mongu, ku Solwezi,
Ku Livingstone na Kaputa,
Tikufuna chitukuko, chifike m'madera onse.