Frobits
🎵 A song made on Frobits

Namwali Tidzakhale Limodzi

0:000:00
Download
Make your own song
Continues securely on the web
Lyrics

Chonde ine ndikupempha, sunga malonjezo
Omwe tinalonjezana, usadzasithe iwe
Pomwe ndili kundende, nkhawa yanga biiii
Kuganizila iwe, ndidzapange bwanji ine
Kuti ndidzatuluke, ndidzakuone iwe
Ngati unasunga malonjezo anthu aja
Chonde, sunga zomwe tinalonjezana
Kuti tidzakhaleso limodzi, limodzi
Namwali, ndiwetu wanga iwe
Eeeee, Namwali tidzakhale limodzi
Pamavuto ndipamtendele iweee
Eeeee Namwali tidzakhale limodzi
Wina afune olo asafune
Eee Tidzakhale limodzi
Kunjaku aliko amuna owoneka bwino
Ndiso achuma chawo asadzakunamize iwe
Kuti mwamuna wako sadzabwelaso
Adzafela komko, uyiwale uyiwale
Koma iwe ndi wanga, chonde sunga moyo wako
Mumboswe mwanga, ndi mmmmm
Pangakhalitse bwanji, zingavute bwanji
Iwe ndiwe wanga, sudzachoka mumtima mwanga
Umakhala mumtima mwanga unamela mizu
Mumtima mwanga, chonde sunga zomwe tinalonjezana
Kuti tidzakhaleso limodzi
Namwali, tidzakhale limodzi
Namwali ndiwetu wanga iwe
Eeeee Namwali tidzakhale limodzi
Wina afune olo asafune
Eeeee Namwali tidzakhale limodzi
RASHID, RASHID, RASHID
S.R.D, S.R.D, S.R.D

More songs by SRD Listen to songs created by others
FROBITS