Ulendo song
*Verse 1*
Pano padziko sipatu
Pano padziko ndise alendo
Koma tilinakwatu kuja ku Jerusalem
Mai wanga ndise alendo
Tate wanga ndise alendo
Sister, brother, pano padziko sipathu oh oh ndise alendo
*Verse 2*
Tikuyenda m’njira yovuta
Minga ndi mitengo zimatilasa
Koma tidzapirira mpaka kuja ku Jerusalemu
Mai wanga tipirire
Tate wanga tipirire
Sister, brother, tidzapirira mpaka kuja ku Jerusalemu
*Verse 3*
Dziko lino ladzala ndi zowawa
Misodzi ndi kulira kulipo
Koma ku Kumwamba kuli chimwemwe chosatha
Mai wanga musalire
Tate wanga musalire
Sister, brother, ku Kumwamba kuli chimwemwe chosatha
*Verse 4*
Yesu akutidikira
Ndi manja otambasula
Akuti “Bwerani ana anga, mupezempumulo”
Mai wanga tiyeni
Tate wanga tiyeni
Sister, brother, yesu akudikira