Frobits
🎵 A song made on Frobits

Paphiri Ndipadambo Ponsepo Pali Mlungu

0:000:00
Download
Reply with a song
Lyrics

Chorus
Paphiri ndipadambo
Ponsepo pali Mlungu,
Poyenda ife m'njira
Poima pali Mlungu; ......oooh Paphiri
Paphiri ndipadambo
Ponsepo pali Mlungu,
Poyenda ife m'njira
Poima pali Mlungu;
Verse 1
Ndi maso Ambuyathu
Apenyetsetsa ife;
Amadalits onse
Okhulupirira Iye;
Amamva timbalame,
Namveka dziko lonse;
Sataya tizilombo,
Asunga zina zonse.
Chorus
Paphiri ndipadambo
Ponsepo pali Mlungu,
Poyenda ife m'njira
Poima pali Mlungu; ......oooh Paphiri
Paphiri ndipadambo
Ponsepo pali Mlungu,
Poyenda ife m'njira
Poima pali Mlungu;
Verse 2
Okwawa pansi inu,
Oyenda m'maddzi inu;
Oyesa dziko nkwanu,
Am'mlengalenga inu,
Nonsenu ntchito zake
Muona tsiku n'tsiku,
Saleka kusamala
Ndi kudalitsa inu.
Chorus
Paphiri ndipadambo
Ponsepo pali Mlungu,
Poyenda ife m'njira
Poima pali Mlungu; ......oooh Paphiri
Paphiri ndipadambo
Ponsepo pali Mlungu,
Poyenda ife m'njira
Poima pali Mlungu;
Verse 3
Nditama mphamvu yake
Ya Mlungu yondizinga;
N'kafoka an'limbitsa,
N'kadwala andichiza.
Pakundisiya bwenzi
Mulungu ali paja;
N'kalowa imfa ine
Alipo Mlungu wanga
Chorus
Paphiri ndipadambo
Ponsepo pali Mlungu,
Poyenda ife m'njira
Poima pali Mlungu; ......oooh Paphiri
Paphiri ndipadambo
Ponsepo pali Mlungu,
Poyenda ife m'njira
Poima pali Mlungu;

More songs by Mike Listen to songs created by others
FROBITS