Title: Mundubile na Makebi
(Chorus)
Mundubile na Makebi, tiomboleni ku mdima,
Banatipeleka ku usiku, tasoba kolirira.
Mundubile na Makebi, tiyatsileni nyale,
Tione poponda bwino, chitukuko chifike konse.
Ku Mongu, ku Solwezi,
Ku Livingstone na Kaputa,
Tiyatsileni nyale, chitukuko chilowe muchipata.
(Verse 1)
Banatilonjeza mbandakucha, dzuwa lidzawala,
Koma kholoko yaima pa zero, nthawi siyiyenda.
Anati zinthu zisintha, moyo uzakhala bwino,
Koma lero tikufunsa, kodi lonjezolo lili kuti?
(Chorus)
Mundubile na Makebi, tiyatsileni nyale,
Tione poponda bwino, chitukuko chifike konse.
Ku Mongu, ku Solwezi,
Ku Livingstone na Kaputa,
Tiyatsileni nyale, chitukuko chilowe muchipata.
(Verse 2)
Banati nkhuku tizadya, unga ukhale wotsika,
Fuel na dollar zibwerera, moyo ukhale wosavuta.
Koma lero mdima wokha, malonjezo anangotha,
Tatsala ndi mafunso ambiri, mayankho palibe.
(Verse 3)
Beve kwao chabe ophunzira, m'ma province onse,
Police commissioners ambiri, ochokera mbali imodzi.
Data base recruitment inayima, achinyamata akuyembekezabe,
Anasiliza sukulu kalekale, ntchito azalowa liti?
(Chorus)
Mundubile na Makebi, tiyatsileni nyale,
Tione poponda bwino, chitukuko chifike konse.
Ku Mongu, ku Solwezi,
Ku Livingstone na Kaputa,
Tiyatsileni nyale, chitukuko chilowe m'zipata.
(Verse 4)
Migodi anagulitsa, anthu akufunsa chifukwa,
Ndalama zikupita kuti? ndani akupindulapo?
Lero aletsa campaign Ku Kaputa, mawu akuchuluka,
Koma anthu aku Magoye akufunsa, "Tawama pati?"
(Final Chorus)
Mundubile na Makebi, tiomboleni ku mdima,
Tiyatsileni nyale lero, tione njira ya mawa.
Ku Mongu, ku Solwezi,
Ku Livingstone na Kaputa,
Tikufuna chitukuko, chifike m'madera onse.